1 Kings 22:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chinanso ndiye kuti Yehosafati adapirikitsa gulu lotsalira la anthu ochitana zadama ku malo achipembedzo, amene anali adakalipo pa nthaŵi ya Asa, bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachotsa m'dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wake Asa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zachiwerewere mwa chipembedzo amene anatsalira pa nthawi ya ulamuliro wa Asa, abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacotsa m'dziko anyamata onyansa aja adatsalira masiku a atate wace Asa.