1 Kings 22:48 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehosafati adapanga zombo zazikulu zomapita ku Ofiri kukatenga golide. Koma zombozo sizidayende chifukwa zidaaonongeka ku Eziyoni-Gebere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehosafati anamanga zombo za ku Tarisisi kukatenga golide ku Ofiri; koma sizinamuka, popeza zinaphwanyika pa Eziyoni-Gebere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehosafati anapanga sitima zapamadzi zopita ku Ofiri kukatenga golide, koma sitimazo sizinayende chifukwa zinawonongeka ku Ezioni Geberi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehosafati anamanga zombo za ku Tarsisi kukatenga golidi ku Ofiri; koma sizinamuka, popeza zinaphwanyika pa Ezioni Geberi.