1 Kings 22:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahaziya mwana wa Ahabu, adauza Yehosafati kuti, “Amalinyero anga apite limodzi ndi amalinyero anu pa zombo.” Koma Yehosafati sadavomere zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Ahaziya mwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m'zombo. Koma Yehosafati anakana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo Ahaziya mwana wa Ahabu anawuza Yehosafati kuti, “Anthu anga ayende pa madzi pamodzi ndi anthu anu,” koma Yehosafati anakana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Ahaziyamwana wa Ahabu ananena ndi Yehosafati, Anyamata anga amuke pamodzi ndi anyamata anu m'zombo. Koma Yehosafati anakana.