1 Kings 22:51 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahaziya mwana wa Ahabu, adaloŵa ufumu wa Ku Israele ku Samariya pa chaka cha 17 cha ufumu wa Yehosafati, mfumu ya ku Yuda. Ndipo adalamulira anthu a ku Israele zaka ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahaziya mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya ku Israeli ku Samariya mʼchaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israyeli pa Samaria m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri ca Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.