1 Kings 22:52 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo ankachita zoipa pamaso pa Chauta, ankatsata mayendedwe oipa a atate ake ndi amai ake. Ankatsatanso zoipa za Yerobowamu, mwana wa Nebati, amene ankachimwitsa kwambiri anthu a ku Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachita choipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wake, ndi ya amake, ndi ya Yerobowamu mwana wa Nebati, amene adachimwitsa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, chifukwa anayenda mʼnjira za abambo ndi amayi ake komanso mʼnjira za Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacita coipa pamaso pa Yehova, nayenda m'njira ya atate wace, ndi ya amace, ndi ya Yerobiamu mwana wa Nebati, amene adacimwitsa Israyeli.