1 Kings 22:53 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahaziyayo ankatumikira Baala ndi kumampembedza, ndipo potero adaputa mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele, potsata zonse zimene atate ake ankachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natumikira Baala, namweramira, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele, monga umo anachitira atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Potumikira ndi kupembedza Baala, iye anakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli, monga momwe anachitira abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natumikira Baala, namweramira, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israyeli, monga umo anacitira atate wace.