1 Kings 22:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahabu adasonkhanitsa aneneri ake okwanira ngati 400, ndipo adaŵafunsa kuti, “Kodi ndipite kukamenyana nkhondo ndi Ramoti-Giliyadi, kaya kapena ndileke?” Aneneriwo adamuuza kuti, “Pitani, pakuti Ambuye aupereka mzindawo kwa inu mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mfumu ya Israeli inasonkhanitsa pamodzi aneneri okwanira 400, ndipo inawafunsa kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena ndileke?” Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Ambuye waupereka mzindawo mʼmanja mwa mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu ya Israyeli inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Gileadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.