1 Kings 22:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahabu adauza Yehosafati kuti, “Alipo munthu wina amene angapemphe nzeru kwa Chauta, dzina lake ndi Mikaya, mwana wa Imila. Koma ine ndimadana naye ameneyo popeza kuti sandilosera zabwino koma zoipa.” Tsono Yehosafati adati, “Iyai mfumu, msatero.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya ku Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife tingakafunsire kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa iyeyo samanenera kanthu kalikonse kabwino ka ine, koma zoyipa nthawi zonse. Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.” Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu musatero.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wace wa Yimla. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.