1 Kings 3:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni adapalana chibwenzi ndi Farao mfumu ya ku Ejipito pokwatira mwana wa Faraoyo. Adabwera naye mkaziyo ku mzinda wa Davide ku Yerusalemu, nakhala naye komweko mpaka atamaliza kumanga nyumba yake yatsopano ndi Nyumba ya Chauta ndiponso linga lozungulira mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumudzi wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anachita ubale ndi Farao mfumu ya ku Igupto ndipo anakwatira mwana wake wamkazi. Mkaziyo anabwera naye mu Mzinda wa Davide mpaka anatsiriza kumanga nyumba yaufumu ndi Nyumba ya Yehova ndiponso khoma lozungulira Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aigupto, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye ku mudzi wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.