1 Kings 3:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mulungu adauza Solomoni kuti, “Chifukwa chakuti wapempha zimenezi, osapempha moyo wautali kapena chuma kapena imfa ya adani ako, koma nzeru zolamulira anthu bwino,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu anati kwa iye, Popeza wapempha chimenechi, osadzipemphera masiku ambiri, osadzipempheranso chuma, osadzipempheranso moyo wa adani ako, koma wadzipemphera nzeru zakumvera milandu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu anati kwa iye, Popeza wapempha cimeneci, osadzipemphera masiku ambiri, osadzipempheranso cuma, osadzipempheranso moyo wa adani ako, koma wadzipemphera nzeru zakumvera mirandu;