1 Kings 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndiye Ine ndikuchitira zimene wapempha. Zoona, ndikupatsa mtima wanzeru ndi waluntha, kotero kuti sadaonekepo nkale lonse wina wofanafana nawe, ndipo sadzaonekanso wina wolingana nawe, iweyo utafa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
taona, ndacita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka.