1 Kings 3:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi woyamba adati, “Inu mbuyanga, ine ndi mnzangayu timakhala nyumba imodzi. Tsono ine ndidaona mwana, mnzangayu ali m'nyumba momwemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi mmodzi anati, Mbuye wanga, ine ndi mkazi uyu tikhala awiri m'nyumba imodzi; ndipo ine ndinaona mwana, iye ali m'nyumbamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi mwa amayiwo anati, “Mbuye wanga, mayi uyu ndi ine timakhala nyumba imodzi. Ine ndinabala mwana tili limodzi ndi mnzangayu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi mmodzi anati, Mbuye wanga, ine ndi mkazi uyu tikhala awiri m'nyumba imodzi; ndipo ine ndinaona mwana, iye ali m'nyumbamo.