1 Kings 3:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lachitatu lake, ine nditachira kale, mnzangayu nayenso adaona mwana. Ndipo ifeyo tinali tokha, panalibe munthu wina aliyense m'nyumbamo, koma aŵiri tokhafe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika kuti tsiku lachitatu nditaona ine mwana, mnzangayu anaonanso mwana; ndipo ife tinali pamodzi, munalibe mlendo ndi ife m'nyumbamo, koma ife awiri m'nyumbamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lachitatu ine nditabala mwana, mnzangayunso anabereka mwana wake. Tinalipo awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe wina aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika kuti tsiku lacitatu nditaona ine mwana, mnzangayu anaonanso mwana; ndipo ife tinali pamodzi, munalibe mlendo ndi ife m'nyumbamo, koma ife awiri m'nyumbamo.