1 Kings 3:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono iyeyu adadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga namgoneka kumimba kwake, ndipo adagoneka mwana wake wakufayo kumimba kwanga. Nthaŵiyo nkuti mdzakazi wanune ndili m'tulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye anauka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga, mdzakazi wanu ndili m'tulo, namuika m'mfukato mwake, naika mwana wake wakufa m'mfukato mwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono iyeyu anadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga ku mimba kwanga pamene ine mdzakazi wanu ndinali mʼtulo. Anamuyika mwanayo ku mimba kwake ndi kuyika mwana wake wakufayo ku mimba kwanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anauka pakati pa usiku, natenga mwana wanga kumimba kwanga, mdzakazi wanu ndiri m'tulo, namuika m'mfukato mwace, naika mwana wace wakufa m'mfukato mwanga.