1 Kings 3:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mkazi wina uja adamdula pakamwa nati, “Iyai, mwana wamoyoyu ndiye wanga, wako ndi wakufayu.” Mkazi woyamba uja adati, “Iyai, mwana wakufayu ngwako, koma wamoyoyu ngwanga.” Adaatero kulankhula kwake azimaiwo pamaso pa mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi winayo anati, Iai, koma wamoyoyu ndi mwana wanga, ndi wakufayu ndi mwana wako. Ndipo uja anati, Iai, koma wakufayu ndi mwana wako, ndi wamoyoyu ndi mwana wanga. Motero iwo analankhula pamaso pa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mayi winayo anati, “Ayi! Mwana wamoyoyu ndi wanga, mwana wakufayu ndi wako.” Koma mayi woyambayo analimbikira kuti. “Ayi! Mwana wakufayu ndi wako; wamoyoyu ndi wanga.” Motero akaziwa anatsutsana pamaso pa mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi winayo anati, lai, koma wamoyoyu ndi mwana wanga, ndi wakufayu ndi mwana wako. Ndipo uja anati, lai, koma wakufayu ndi mwana wako, ndi wamoyoyu ndi mwana wanga. Motero iwo analankhula pamaso pa mfumu.