1 Kings 3:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu idati, “Wina akuti, ‘Mwana wamoyoyu ngwanga,’ winanso akuti, ‘Iyai, mwana wako ngwakufayu, wanga ngwamoyoyu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono mfumu inati, Uyu akuti, Wamoyoyu ndiye mwana wanga ndi wakufayu ndiye mwana wako; ndipo winayo akuti, Iai, koma mwana wako ndiye wakufayu, ndi mwana wanga ndiye wamoyoyu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono mfumu inati, Uyu akuti, Wamoyoyu ndiye mwana wanga ndi wakufayu ndiye mwana wako; ndipo winayo akuti, lai, koma mwana wako ndiye wakufayu, ndi mwana wanga ndiye wamoyoyu.