1 Kings 3:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo mai amene anali mwini wake wa mwana wamoyoyo adagwidwa ndi chisoni chachikulu mu mtima chifukwa cha mwanayo. Choncho adauza mfumuyo kuti, “Pepani, mbuyanga, ingompatsani iyeyu mwana wamoyoyu, musamuphe, ndakupembani.” Koma mai wina uja adati, “Iyai asapatse ine kapena iwe, amdule pakati basi!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mkazi amene mwana wamoyo anali wake analankhula ndi mfumu, popeza mtima wake unalira mwana wake, nati, Ha? Mbuye wanga, mumpatse uyo mwana wamoyo osamupha konse. Koma winayo anati, Asakhale wanga kapena wako, dulani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayi amene mwana wake anali moyo anagwidwa ndi chisoni chifukwa cha mwana wakeyo ndipo anawuza mfumu kuti, “Chonde mbuye wanga, mupatseni mnzangayu mwana wamoyoyu! Musamuphe!” Koma winayo anati, “Ayi, asandipatse ine kapena iwe. Muduleni pakati!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mkazi amene mwana wamoyo anali wace analankhula ndi mfumu, popeza mtima wace unalira mwana wace, nati, Ha! mbuye wanga, mumpatse uyo mwana wamoyo osamupha konse. Koma winayo anati, Asakhale wanga kapena wako, dulani.