1 Kings 3:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Aisraele onse adamva za m'mene mfumu idagamulira mlanduwo. Motero anthu adayamba kulemekeza Solomoni, chifukwa adaona kuti anali ndi nzeru za Mulungu zoweruza mwachilungamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aisraele onse anamva maweruzidwe ake idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Aisraeli onse anamva za chigamulo chimene mfumu inapereka, anaopa mfumuyo kwambiri, chifukwa anaona kuti mfumu inali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu zoweruzira mwachilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aisrayeli onse anamva maweruzidwe ace idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.