1 Kings 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsopano, Inu Chauta Mulungu wanga, mwaika mtumiki wanune pa malo a Davide bambo wanga, ngakhale ndine mwana wamng'ono chabe, ndipo sindidziŵa kagwiridwe kake ka ntchito yanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kutuluka kapena kulowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, Yehova Inu Mulungu wanga, mwalonga ine kapolo wanu ufumu m'malo mwa atate wanga Davide, koma ine ndine kamwana, sindidziwa kuturuka kapena kulowa.