1 Kings 4:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Benigebere ankayang'anira ku Ramoti-Giliyadi ndi midzi ya Yairo mwana wa Manase, imene ili ku Giliyadi. Analinso ndi chigawo cha Aigobu, chimene chili ku Basani, mizinda yaikulu 60 yokhala ndi malinga ndiponso zitseko zamkuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo midzi ya Yairi mwana wa Manase ili m'Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili m'Basani, midzi yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Beni-Geberi, anali woyangʼanira Ramoti Giliyadi (midzi ya Yairi inali ya mwana wa Manase ku Giliyadi, pamodzinso ndi chigawo cha Arigobu ku Basani ndiponso mizinda yake yayikulu makumi asanu ndi umodzi yokhala ndi malinga ndi mipiringidzo yamkuwa).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Benigeheri ku Ramoti Gileadi, iyeyo anali nayo midzi ya Yairo mwana wa Manase iri m'Gileadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobi liri m'Basani, midzi yaikuru makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;