1 Kings 4:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ayuda ndi Aisraele anali ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Anali okondwa chifukwa anali ndi zakudya ndi zakumwa zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ayuda ndi Aisraele anachuluka ngati mchenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a ku Yuda ndi ku Israeli anali ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Ankadya ndi kumwa ndipo ankasangalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ayuda ndi Aisrayeli anacuruka ngati mcenga wa kunyanja, namadya namamwa namakondwera.