1 Kings 4:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni ankalamulira maiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a Ejipito. Maikowo ankakhoma msonkho ndi kumatumikira Solomoni pa masiku onse a moyo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni analamulira maiko onse, kuyambira ku Yufurate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Ejipito; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomoni masiku onse a moyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Solomoni analamulira mayiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a dziko la Igupto. Mayikowa ankabweretsa mphatso ndipo anali pansi pa ulamuliro wa Solomoni moyo wake wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo analamulira maiko onse, kuyambira ku Firate kufikira ku dziko la Afilisti ndi ku malire a Aigupto; anthu anabwera nayo mitulo namtumikira Solomo masiku onse a moyo wace.