1 Kings 4:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho nthaŵi yonse Solomoni ali moyo anthu a ku Yuda ndi a ku Israele anali paufulu, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pamtendere, osasoŵa kanthu kalikonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi ya Solomoni, Yuda ndi Israeli anali pa mtendere, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pansi pa mpesa wake ndi mtengo wake wa mkuyu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wace ndi mkuyu wace, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.