1 Kings 4:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono nduna khumi ndi ziŵiri zija zinkapereka chakudya cha mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadzadya nao kunyumba kwa mfumu, nduna iliyonse mwezi wake. Ndunazo sizinkalola kuti kanthu kalikonse kasoŵe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akapitao aja anatengetsera chakudya Solomoni ndi anthu onse akudya ku gome la mfumu Solomoni, munthu yense m'mwezi mwake, sanalole kanthu kasoweke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abwanamkubwa a zigawo aja, aliyense pa mwezi wake, ankapereka chakudya cha Mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadya naye. Iwo ankaonetsetsa kuti pasasowe kalikonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akapitao aja anatengetsera cakudya Solomo ndi anthu onse akudya ku gome la mfumu Solomo, munthu yense m'mwezi mwace, sanalola kanthu kasoweke.