1 Kings 4:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo anali wanzeru kuposa anthu ena onse, kuposa ngakhale Etani wa ku Ezara, kuposanso Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake idamveka kwa anthu a mitundu yonse yozungulira dziko lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezara, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yake inafikira amitundu onse ozungulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anali wanzeru kuposa munthu wina aliyense, kuposa ngakhale Etani wa banja la Ezara, Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake inamveka kwa mitundu yonse ya anthu ozungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti anali wanzeru woposa anthu onse, woposa Etani wa ku Ezra, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Darida ana a Maholi; ndipo mbiri yace inafikira amitundu onse ozungulira.