1 Kings 4:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero anthu ankabwera kwa Solomoni kuchokera ku maiko onse, kuti adzamve nzeru zake. Ankatumizidwa ndi mafumu onse a pa dziko lapansi amene anali atamva mbiri ya nzeru zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafikapo anthu a mitundu yonse kudzamva nzeru ya Solomoni, ochokera kwa mafumu onse a dziko lonse lapansi, amene adamva mbiri ya nzeru yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a mitundu yonse ankabwera kudzamva nzeru za Solomoni. Anthu amenewa ankatumizidwa ndi mafumu onse a dziko lapansi amene anamvapo za nzeru zakezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafikako anthu a mitundu yonse kudzamva nzeru ya Solomo, ocokera kwa mafumu onse a dziko lonse lapansi, amene adamva mbiri ya nzeru yace.