1 Kings 4:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni anali ndi nduna khumi ndi ziŵiri zimene adaziika m'zigawo zonse za dziko la Israele. Nduna zimenezi zinkapereka chakudya kwa mfumu ndi banja lake lonse. Nduna iliyonse inkapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisraele onse, akufikitsira mfumu ndi banja lake zakudya; aliyense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa chaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni analinso ndi abwanamkubwa khumi ndi awiri amene ankayangʼanira zigawo zonse za dziko la Israeli. Iwo ankapereka chakudya kwa mfumu ndiponso ku banja laufumu. Bwanamkubwa aliyense ankapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisrayeli onse, akufikitsira mfumu ndi banja lace zakudya; ali yense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa caka.