1 Kings 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Hiramu mfumu ya ku Tiro adatuma akazembe ake kwa Solomoni, atamva kuti adamdzoza ufumu m'malo mwa bambo wake, poti Hiramuyo ankakondana ndi Davide nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Hiramu mfumu ya ku Tiro anatuma anyamata ake kwa Solomoni, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wake; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hiramu mfumu ya ku Turo atamva kuti Solomoni wadzozedwa kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo ake Davide, anatumiza akazembe ake kwa Solomoni, chifukwa mfumu Hiramu inali pa ubale wabwino ndi Davide nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Hiramu mfumu ya ku Turo anatuma anyamata ace kwa Solomo, popeza anamva kuti adamdzoza mfumu m'malo mwa atate wace; pakuti Hiramu adakondana ndi Davide masiku onse.