1 Kings 5:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Solomoni adapatsa Hiramu tirigu wokwanira mitanga 20,000 kuti akhale chakudya cha anthu ake, ndiponso mafuta oyenga bwino okwanira mbiya zikuluzikulu 20,000. Ankapereka zimenezi kwa Hiramu chaka ndi chaka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lake, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomoni anapatsa Hiramu chaka ndi chaka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Solomoni anamupatsa Hiramu mitanga ya tirigu 20,000 ngati chakudya cha pa nyumba yake, kuwonjezera pa migolo ya mafuta a olivi yokwana 20,000. Solomoni anapitiriza kupereka zimenezi chaka ndi chaka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anapatsa Hiramu miyeso ya tirigu zikwi makumi awiri ndiyo zakudya za banja lace, ndi miyeso makumi awiri ya mafuta oyera; motero Solomo anapatsa Hiramu caka ndi caka.