1 Kings 5:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankaŵatuma ku Lebanoni anthu 10,000 pamwezi, mosinthanasinthana. Ku Lebanoni ankakhalako mwezi umodzi, ndipo kwao ankakhalako miyezi iŵiri. Adoniramu ndiye amene ankayang'anira ntchito yathangatayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anawatuma ku Lebanoni mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebanoni, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ankatumiza anthu 10,000 ku Lebanoni pa mwezi mosinthanasinthana, kotero kuti ankakhala ku Lebanoniko mwezi umodzi ndipo kwawo ankakhalako miyezi iwiri. Adoniramu ndiye ankayangʼanira ogwira ntchito yathangatayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anawatuma ku Lebano mwezi umodzi zikwi khumi kuwasintha, mwezi umodzi iwo anali ku Lebano, miyezi iwiri anali kwao; ndipo Adoniramu anali kapitao wa athangata.