1 Kings 5:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu idalamula kuti anthuwo akumbe ndi kusema miyala ikuluikulu yabwino kwabasi, yoti akamangire maziko a Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuluikulu ya mtengo wapatali, kuika maziko ake a nyumbayo ndi miyala yosemasema.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Molamulidwa ndi mfumu, anakumba ndi kusema miyala ikuluikulu kwambiri yoti akamangire maziko a Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuru-ikuru ya mtengo wapatali, kuika maziko ace a nyumbayo ndi miyala yosemasema.