1 Kings 5:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amisiri omanga a Solomoni, pamodzi ndi a Hiramu, ndiponso anthu a ku Gebala, ndiwo amene ankasema miyala, ndi kukonza mitengo ndi miyala yomangira Nyumbayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo omanga nyumba a Solomoni ndi omanga nyumba a Hiramu ndi anthu a ku Gebala anaisema, naikonza mitengo ndi miyala yakumangira nyumbayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amisiri a Solomoni ndi a Hiramu ndiponso anthu a ku Gebala anasema miyala ndi kukonza matabwa ndi miyala yomangira Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo omanga nyumba a Solomo ndi omanga nyumba a Hiramu ndi anthu a ku Gebala anaisema, naikonza mitengo ndi miyala yakumangira nyumbayo.