1 Kings 5:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mukudziŵa kuti Davide, bambo wanga, sadathe kumangira nyumba Chauta Mulungu wake, chifukwa cha nkhondo zomwe adani ake adaamzinga nazo mbali zonse. Koma potsiriza Chauta adapereka adani akewo mu ulamuliro wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wake nyumba, chifukwa cha nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu mukudziwa kuti chifukwa cha nkhondo zimene zinkachokera ku mbali zonse kulimbana ndi abambo anga, iwo sanathe kumangira Nyumba Yehova Mulungu wawo, mpaka Yehova atawayika adani awo pansi pa ulamuliro wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudziwa inu kuti atate wanga Davide sanathe kumangira dzina la Yehova Mulungu wace nyumba, cifukwa ca nkhondo zakumzinga konseko, mpaka atawaika Yehova pansi pa mapazi ace.