1 Kings 5:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Hiramu atamva mau a Solomoniwo, adakondwa kwambiri, ndipo adati, “Lero Chauta atamandike chifukwa adapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu wotchukawu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika, pamene Hiramu anamva mau ake a Solomoni, anakondwera kwakukulu, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hiramu anakondwa kwambiri atamva uthenga wa Solomoni ndipo anati, “Lero Yehova atamandike chifukwa wapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu waukuluwu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika, pamene Hiramu anamva mau ace a Solomo, anakondwera kwakukuru, nati, Alemekezeke Yehova lero amene wampatsa Davide mwana wanzeru akhale mfumu ya anthu aunyinji amenewa.