1 Kings 5:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu anga adzatsika nayo kuchokera kuno ku Lebanoni mpaka ku nyanja. Ndipo adzaiyandamitsa pa madzi pa phaka, kuti apite nayo ku malo amene munene. Tsono adzaimasulira kumeneko, ndipo inu mudzailandira. Chofuna ine nchongoti inuyo mudzandipatse chakudya chodyetsa anthu anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebanoni kufika nayo ku nyanja, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzachita chifuniro changa, kumapatsa banja langa zakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anga adzatsika nayo kuchokera ku Lebanoni mpaka ku nyanja, ndipo adzayiyandamitsa pa nyanja mpaka ku malo amene munene. Kumeneko ndidzayimasula ndipo mudzayitenga. Ndipo inu mudzakwaniritsa chokhumba changa pondipatsa chakudya cha banja langa laufumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akapolo anga adzatsika nayo ku Lebano kufika nayo ku nyanja yamcere, ndipo ine ndidzaiyandamitsa paphaka kufikira komwe mudzandiuzako, ndi kumeneko ndidzaimasula, ndipo mudzaitenga; nimudzacita cifuniro canga, kumapatsa banja langa zakudya.