1 Kings 6:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakutha pa zaka 480 Aisraele atatuluka ku Ejipito, chaka chachinai cha ufumu wa Solomoni wolamulira Aisraele, pa mwezi wa Zivi, umene uli mwezi wachiŵiri, Solomoni adayambapo kumanga Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patapita zaka 480 Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto, chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomoni mu Israeli, mwezi wa Zivi, umene ndi mwezi wachiwiri, Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu ataturuka ana a Israyeli m'dziko la Aigupto, caka cacinai cakukhala Solomo mfumu ya Israyeli, m'mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi waciwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.