1 Kings 6:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kunena za Nyumba ukumangayi, iwe ukamamvera mau anga ndi malangizo anga ndi kutsata malamulo anga onse, Ine ndidzakuchitiradi zimene ndidalonjeza kwa Davide bambo wako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunena za nyumba yino ulikuimanga, ukamayenda iwe m'malemba anga, ndi kumachita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kunena za Nyumba imene ukumangayi, ngati iwe udzamvera malangizo anga ndi kutsatira mawu anga, ngati udzasunga malamulo anga ndi kuwachita, Ine ndidzakwaniritsa zonse zomwe ndinalonjeza Davide abambo ako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunena za nyumba yino ulikuimanga, ukamayenda iwe m'malemba anga, ndi kumacita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako.