1 Kings 6:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake makoma a Nyumba ya Chauta m'kati mwake Solomoni adaŵachinga ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi pa Nyumbayo mpaka ku siling'i. Pansi pake pa Nyumbayo adayalapo matabwa apaini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatchinga makoma a nyumba m'katimo ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi kufikira posanja, natchinga m'katimo ndi matabwa, nayala pansi m'nyumbamo matabwa amlombwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anakuta khoma la mʼkati mwake ndi matabwa a mkungudza, kuyambira pansi pa Nyumbayo mpaka ku denga ndipo pansi pa Nyumbayo anayalapo matabwa a payini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacinga makoma a nyumba m'katimo ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi kufikira posanja, nacinga m'katimo ndi matabwa, nayala pansi m'nyumbamo matabwa amlombwa.