1 Kings 6:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbuyo kwa Nyumbayo adadula chipinda kutalika kwake mamita asanu ndi anai. Adachimanga ndi matabwa amkungudza kuyambira pansi mpaka ku siling'i. Chipindachi adachimanga m'kati mwa Nyumbayo, kuti chikhale chipinda chopatulika cham'kati, malo opatulika kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwake, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ichi anamanga kukhala chipinda chamkati, malo opatulika kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbuyo kwa Nyumbayo anadula chipinda chachitali mamita asanu ndi anayi. Chipindachi anachimanga ndi matabwa a mkungudza kuyambira pansi mpaka ku denga kuti chikhale chipinda chopatulika chamʼkati mwa Nyumba ya Mulungu ngati Malo Wopatulika Kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m'kati mwa nyumba m'tsogolo mwace, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ici anamanga m'katimo cikhale monenera, malo opatulikitsa.