1 Kings 6:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'kati mwa Nyumbayo pa matabwa amkungudza aja adajambulapo zithunzi za zikho ndi za maluŵa. Ponse panali mkungudza wokhawokha, miyala ya khoma osaoneka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gada; munali mikungudza yokhayokha simunaoneka mwala ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼkati mwa Nyumbayi munali matabwa a mkungudza, pamene anajambulapo zithunzi za zikho ndi maluwa. Paliponse panali mkungudza wokhawokha. Panalibe mwala uliwonse umene unkaonekera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gada; munali mikungudza yokha yokha simunaoneka mwala ai,