1 Kings 6:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyumba imene mfumu Solomoni adamangira Chauta muutali mwake inali ya mamita 27, muufupi mwake inali ya mamita asanu ndi anai, ndipo msinkhu wake unali wa mamita pafupi 13 ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nyumbayo mfumu Solomoni anaimangira Yehova, m'litali mwake munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyumba imene Solomoni anamangira Yehova mulitali mwake inali mamita 27, mulifupi mwake inali mamita asanu ndi anayi, ndipo msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nyumbayo mfumu Solomo anaimangira Yehova, m'litali mwace munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m'mimba mwace mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace mikono makumi atatu.