1 Kings 6:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Solomoni adakuta golide weniweni m'kati mwake mwa Nyumbayo, ndipo adalambalika maunyolo agolide mopingasitsa kutsogolo kwa chipinda chopatulika cham'kati naŵakuta ndi golide. Chipinda chimenechinso chidakutidwa ndi golide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo Solomoni anakuta m'kati mwa nyumba ndi golide woyengetsa, natambalika maunyolo agolide chakuno cha chipinda chamkati, namukuta ndi golide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anakutira golide weniweni mʼkati mwake mwa Nyumbayi, ndipo anayalika maunyolo a golide mopingasa kutsogolo kwa malo wopatulika amene anakutidwa ndi golide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo Solomo anakuta m'kati mwa nyumba ndi golidi woyengetsa, natambalika maunyolo agolidi cakuno ca monenera, namukuta ndi golidi.