1 Kings 6:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapanga akerubi aŵiri a mtengo wa olivi, msinkhu wa aliyense unali mamita anai ndi theka, ndipo adaŵaika m'chipinda chopatulika cham'kati chija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'chipinda chamkatimo anasema mitengo ya azitona akerubi awiri, yense wa msinkhu wake mikono khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchipinda chopatulika cha mʼkati anapangamo akerubi awiri a mtengo wa olivi. Msinkhu wa kerubi aliyense unali mamita anayi ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'moneneramo anasema mitengo yaazitona akerubi awiri, yense wa msinkhu wace mikono khumi.