1 Kings 6:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Phiko limodzi la kerubi kutalika kwake kunali mamita aŵiri nkanthu, phiko linanso kutalika kwake mamita aŵiri nkanthu. Kufunyulula mapiko aŵiriwo, kuchokera nsonga ina mpaka nsonga ina, kutalika kwake kunali mamita anai ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo phiko limodzi la kerubi linali la mikono isanu, ndi phiko lina la kerubi linalinso la mikono isanu; kuyambira ku nsonga ya phiko limodzi kufikira ku nsonga ya phiko lina inali mikono khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Phiko limodzi la kerubi kutalika kwake kunali mamita awiri ndi theka, phiko linanso linali mamita awiri ndi theka, kutambasula mapiko awiriwo, kuchokera msonga ina mpaka msonga ina kutalika kwake kunali mamita anayi ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo phiko limodzi la kerubi linali la mikono isanu, ndi phiko lina la kerubi linalinso la mikono isanu; kuyambira ku nsonga ya phiko limodzi kufikira ku nsonga ya phiko lina inali mikono khumi.