1 Kings 6:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni adaika akerubiwo m'chipinda cha m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo. Ndipo mapiko ao adaŵatambalitsa kotero kuti phiko limodzi la kerubi mmodzi linkakhudza khoma lina, ndipo phiko limodzinso la kerubi winayo linkakhudza khoma lina. Mapiko enawo ankakhudzana pakati pa Nyumba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaika akerubiwo m'chipinda cha m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lake la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anayika akerubiwo mʼchipinda cha mʼkati mwenimweni mwa Nyumba ya Mulungu, atatambasula mapiko awo. Phiko la kerubi wina limakhudza khoma lina, pamene phiko la winayo limakhudza khoma linanso ndipo mapiko awo amakhudzana pakati pa chipindacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaika akerubiwo m'cipinda ca m'katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lace la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.