1 Kings 6:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adazokota zithunzi za akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluŵa, kuzungulira makoma onse a Nyumbayo, ndiponso m'zipinda zam'kati ndi zakunja zomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nalemba m'makoma onse akuzinga chipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, m'katimo ndi kumbuyo kwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa makoma onse kuzungulira Nyumbayo, mʼzipinda za mʼkati ndi za kunja zomwe, anajambulapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nalemba m'makoma onse akuzinga cipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, m'katimo ndi kumbuyo kwace.