1 Kings 6:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono chipinda chakubwalo m'mimba mwake munali mwa mamita asanu ndi anai, kulingana ndi muufupi mwa Nyumbayo. Kutalika kunali kwa mamita anai ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m'litali mwake munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipinda chakubwalo mʼmbali mwake chinali mamita asanu ndi anayi kulingana ndi mulifupi mwa Nyumbayo ndipo kutalika kwake kunali kwa mamita anayi ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamanga likole pakhomo pa nyumba ya kacisiyo, m'litali mwace munali mikono makumi awiri monga m'mimba mwace mwa nyumbayo, kupingasa kwace kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.