1 Kings 6:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa zitseko ziŵiri zija za mtengo wa olivi adazokotapo zithunzi za akerubi, za mitengo ya mgwalangwa ndi maluŵa. Tsono zitsekozo adazikuta ndi golide, ndipo adapaka golide pa akerubiwo ndi pa mitengo ya mgwalangwa ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo wa azitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nawakuta ndi golide; inde anakutanso ndi golide akerubi ndi migwalangwayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pa zitseko ziwiri zija za mtengo wa olivi anajambulapo kerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa ndipo anapaka golide akerubiwo ndi mitengo ya mgwalangwayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo waazitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nawakuta ndi golidi; inde anakutanso ndi golidi akerubi ndi migwalangwayo.