1 Kings 6:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pa chaka cha 11 mwezi wa Buli, mwezi wachisanu ndi chitatu, madera onse a Nyumbayo adatha kumangidwa monga momwe kunkafunikira. Nyumbayo adaimanga pa zaka zisanu ndi ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa chaka cha 11 mwezi wa Buli, mwezi wachisanu ndi chitatu, madera onse a Nyumba anatha kumangidwa monga momwe kunkafunikira. Anamanga Nyumbayo kwa zaka zisanu ndi ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'caka cakhumi ndi cimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wacisanu ndi citatu anatsiriza nyumba konse konse monga mwa mamangidwe ace onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.