1 Kings 6:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyumbayo poimanga, idamangidwa ndi miyala yosemeratu. Choncho pogwira ntchitoyo, sipadamveke nyundo, nkhwangwa kapena chipangizo chilichonse chachitsulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveka kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena chipangizo chachitsulo, pomangidwa iyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Poyimanga Nyumbayo, anagwiritsa ntchito miyala yosemeratu, ndipo pogwira ntchitoyo sipanamveke nyundo, nkhwangwa kapena chida china chilichonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveka: kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena cipangizo cacitsulo, pomangidwa iyo.